Dementia

exp date isn't null, but text field is

Information on Dementia

What is Dementia?

Dementia is a general term used to describe a group of conditions which affect memory.

You find it harder to remember things and develop other problems with your thinking. These make it more difficult to cope with your day to day life.

These problems keep getting worse - or are 'progressive'. They are not a normal part of ageing.

What does dementia feel like?

There are many different types of dementia. They all involve loss of memory, but they also have other symptoms, which differ according to the cause. A dementia will often start off with memory problems, but a person with dementia can also find it hard to:

  • plan and carry out day-to-day tasks
  • communicate with others.

They may also have changes in their mood, ability to make decisions, or you may see changes in their personality.

As dementia is 'progressive', someone with dementia will become more dependent upon others to help them as time goes on.

What causes dementia?

Any of us can develop a dementia but it is not a natural or inevitable consequence of ageing. Some medical conditions that can make it more likely include:

  • Parkinson’s disease
  • Strokes and heart disease
  • High blood pressure and high cholesterol levels
  • Type 2 diabetes mellitus.

It is important to try to treat and manage these risk factors, particularly high blood pressure and diabetes. It may also help, in the mid-life years, to manage any problems with hearing loss, obesity, social isolation and depression.

Genes also play a part in dementia but there is no test (yet) which can predict your personal risk.

Lifestyle factors that can increase risk of various types of dementia include:

  • smoking
  • drinking more than the safe limit of alcohol - more than 14 units per week
  • poor diet
  • lack of physical activity
  • being overweight
  • repeated head injuries, eg in boxers.

As dementia is 'progressive', someone with dementia will become more dependent upon others to help them as time goes on.

How can I get help for dementia?

Simple practical steps

  • Use a diary to help you remember appointments.
  • Make lists of the things you have to do – and tick them off as you do them!
  • Keep your mind active by reading or doing puzzles, learning new things and maintaining a sense of purpose in your life.
  • Stay involved and connected – find your local bao group or other social activities which you enjoy.
  • Eat a healthy diet and take physical exercise (it can help whatever your age).
  • Get support if you are struggling with daily living or get advice if others feel you are finding things hard to manage. There are many ways in which family, friends and services can help you to live independently for as long as possible.

Medication

There are a group of drugs called acetylcholinesterase inhibitors that can slow down the progress of dementia a little, but they are not very effective and not available in Malawi yet.

Uthenga wokhudzana ndi matenda a Dimensha

Kodi matenda a dimensha ndi chani?

Dimensha ndi mawu omwe amagwiritsidwa ntchito pokamba za magulu a matenda okhudzana ndi kukumbukira zinthu.

Munthu odwala matendawa samatha kukumbukira zinthu bwinobwino ndiponso amakhala ndi mavuto mkaganizidwe. Kusakumbukira zinthu komanso mavuto ndi maganizidwewa amapangitsa kuti munthu asapilira ndi zinthu zimene amachita tsiku ndi tsiku.

Mavuto amenewa amanka nakula ndipo sikuti ndimbali yaukalamba.

Kodi zizindikiro za matenda a dimensha ndi chani?

Pali mitundu yambiri ya dimensha. Mitundu yonseyo imakhudzana ndi kakumbukilidwe/kuyiwala kwa zinthu, komanso ali ndi zizindikiro zina, zomwe zimasiyana malingana ndi chomwe chayambitsa matendawa. Dimensha nthawi zambiri imayamba ndi vuto lokumbukira zinthu, koma munthu amene ali ndi matendawa amavutikanso ku:

  • Lingalira ndi kuchita zinthu zomwe amapanga tsiku ndi tsiku
  • Kulumikizana ndi anthu ena.

Amathanso kusintha makhalidwe komanso kulephera kupanga zinthu payekha.

Chifukwa choti matenda a dimensha amanka nakula, munthu amene ali ndi vutoli amapitilira kudalira anthu ena kumuthandizira matsiku akamapita.

Chimayambitsa dimeshia ndichani?

Munthu wina aliyense angathe kudwala dimensha koma tiyenera kuzindikira kuti dimensha sinjira yomwe munthu aliyense amakalambiria. Matenda awa ndi amene nthawi zambiri amayambitsa dimensha:

  • Matenda a manjenje (pakinisoni)
  • Matenda ofa ziwalo komanso mavuto a mtima
  • Matenda othamanga magazi (Bp) komanso okhala ndi Mafuta ambiri
  • Matenda a shuga

Pachifukwachi, nkofunikira kwambiri kuthana ndi ziopsezo zimenezi makamaka kuthamanga kwa magazi (BP) ndi matenda a shuga kuti tipewe dimensha. Zingathenso kuthandiza pamene munthu sunayambe kukalamba kuthana ndi mavuto monga akumva kunenepa kwambiri, kuzipatula komanso matenda okhumudwa.

Majini nawonso amathandizira kwambiri kudwala demesha angakhale nkosatheka kudziwilatu chiopsezo Kamba ka majini munthu ali nawo.

Makhalidwenso angathe kuika munthu pa chiopsezo chodwala matendewa. Makhalidwe amenewa ndi:

  • Kusuta fodya
  • Kumwa mowa mwauchidakwa
  • Madyedwe osakhala bwino
  • Kusapanga masewero olimbitsa thupi
  • Kunenepa kwambiri
  • Kuvulala kumutu kawirikawiri- osewera nkhonya

Chifukwa choti matenda a demesha amanka nakula, munthu amene ali ndi vutoli amapitilira kudalira anthu ena kumuthandizira masiku akamapita.

Ndingapeze bwanji thandizo la matendawa?

Njira za pafupi zoti mungathe kupanga

  • Gwiritsani ntchito kabuku kuti kakuthandizeni kukumbukira zomwe mukufuna kupanga.
  • Lembani mndandanda wa zinthu zomwe mutapange ndipo chongani zomwe mwapanga kale
  • Onetsetsani kuti muli otanganidwa ndi zinthu monga kuwerenga kapena kupanga masewero olemba, kuphunzira zinthu za tsopano
  • Lumikizanani ndi anzanu ndipo muzitengapo gawo mzochitika
  • Idyani chakudya chopatsa thanzi komanso pangani masewero olimbitsa thupi.
  • Kalandileni thandizo ngati mukupeza mavuto osiyanasiyana ndi moyo wanu wa tsiku ndi tsiku komanso kalandileni uphungu ngati anthu ena akuona kuti mukulephera kukwanitsa kupanga zinthu. Pali njira zambiri zomwe abwenzi ndi achibale angathe kukuthandizani kuti mukhale moziyimila panokha

Mankwala 

  • Pali magulu a mankhwala otchedwa acetylcholinesterase inhibitors omwe amathandizira kuchepetsa kukula kwa matendawa koma sikuti amathandiza kwambiri komanso sapezeka kuno ku Malawi