Epilepsy

exp date isn't null, but text field is

Information on Epilepsy

What is epilepsy?

A seizure or ‘fit’ is an episode of symptoms caused by a burst of abnormal electrical activity in the brain that usually lasts from a few seconds to a few minutes. Repeated seizures means that you have epilepsy. 

What does epilepsy feel like?

The severity of a seizure can vary greatly; from spells of absence (staring into space with no movement) to loss of consciousness and violent convulsions. The type of seizure a person has depends on the underlying cause of the seizure.

In a convulsive seizure the whole brain is affected and the person having the seizure becomes unconscious. They may also:

  • Fall to the floor
  • Bite their tongue
  • Become stiff and shake
  • Their eyeballs may roll upwards
  • Froth at the mouth
  • Lose control of their bladder / bowels
  • Their lips may turn blue

In a non-convulsive seizure, the person may be awake but confused or lose touch with their surroundings and may experience the following:

  • Jerky movements in one part of their body (e.g. their arm or leg)
  • Their lips may smack together repeatedly
  • They may stare into space and appear as if they are in a trance (absence seizure)
  • Many persons experience a warning or ‘aura’ that the seizure is about to start, such as hearing, seeing or smelling things which are unusual.

What causes epilepsy?

In many cases, no cause for the seizures can be found. The abnormal bursts of electrical activity in the brain occur for no known reason.

However, any damage to the brain has the potential to cause seizures. Damage is commonly from head injuries (an accident, during childbirth) or infections (HIV, malaria). There is often a family history or genetic component. It is not caused by spirits or witchcraft!

How can I get help for epilepsy?

Simple practical steps

  • People with epilepsy should not take baths or swim alone or cook over an open fire alone in case they harm themselves.
  • People with epilepsy should not drive or operate heavy machinery in case they harm themselves and others

Take steps to avoid your triggers for seizures. Triggers typically include:

  • Stress and anxiety
  • Lack of sleep
  • Heavy alcohol intake or using street drugs
  • Flickering lights such as from video games
  • Irregular meals which may cause low blood sugar levels

Medication

Epilepsy cannot be cured with medication. However, with the right type and strength of medication, the majority of people with epilepsy do not have seizures.

You need to take medication every day to prevent seizures.

Treatment should never be stopped suddenly due to risk of prolonged seizure and maybe death

A trial without medication may be an option if you have not had any seizures over 2-3 years.

If a decision to stop treatment is made, a gradual reduction of the dose of medication is usually advised over several months. You should never stop taking medication without discussing it with a doctor.

Uthenga wokhudzana ndi matenda a Khunyu

Kodi matenda a khunyu ndi chani?

Kugwa chifufu ndi chizindikiro choti muubongomu katumizilidwe ka mauthenga sikakuyenda bwino. Zimenezi zimatenga kanthawi pang’ono (mphindi zochepa chabe). Ngati munthu akugwa chifufu pafupi pafupi, zimatanthauza kuti ali ndimatenda a khunyu.

Kodi matenda a khunyu amakhala bwanji?

Kukula kwa chifufu kungathe kusiyana kwambiri; wodwala ena simungawazindikire kuti akugwa chifufu pamene ena amatha kukomoka kumene kapenanso kumagwa ndi mphamvu. Kotero mtundu wa chifufu umene munthu ali nawo   umatengera ndi chomwe chimayambitsa kugwa chifufu.

Munthu akamagwa chifufu ndi kukomoka, ubongo onse umakhala utakhudzidwa. Munthuyo angathenso:

  • Kugwa pansi
  • Kudziluma lilime
  • Kuuma thupi komanso kumazigwededza kwambiri
  • Kuyang’anitsa maso ake mmwamba
  • Kutuluka thovu kukamwa
  • Kukodzedwa kapena kubibidwa kumene
  • Milomo yawo kusintha mtundu.

Munthu yemwe amagwa mosazionetsera, amatha kukhala maso koma amangosokonekera zochitika komanso sadziwa kuti akuchita chani. Ndipo angathe kuonetsa zinthu izi:

  • Kunjenjemera kwa mbali imodzi ya thupi lawo (monga mwendo kapena mkono)
  • Milomo kumagundana mwapafupipafupi kwambiri
  • Kuyang’anitsitsa malo amodzimodzi
  • Ambiri amakhala ndi chenjezo loti agwa chifufu posachedwa (ngati kumva, kuona kapena kununkhidza zinthu zodabwitsa) choti chifufu chiyamba.

Kodi chimayambitsa matenda a khunyu ndi chani?

Chenicheni chomwe chimayambitsa matendawa nthawi zambiri sichimadziwika. Kusonekera kwa mauthenga mu ubongo kumatha kuchitika popanda chifukwa china chilichonse.

Komabe, kuvulala kwina kulikonse kwa muubongo kuli ndi kuthekera koyambitsa kugwa chifufu. Kuvulala kumeneku nthawi zambiri kumapangika munthu akavulala kumutu (Ngozi, nthawi yobadwa) kapena matenda (HIV, Malungo). Komanso nthawi zambiri pamakhala mbiri kuchokera kwa makolo kapena achibale. Tiyenera kudzindikira kuti matenda a khunyu sayambitsidwa ndi mizimu komanso ufiti!

Thandizo ndingalipeze bwanji la matenda a khunyu?

Njira za pafupi ndi izi

  • Anthu amene amadwala matenda a khunyu asamasambe kapena kukasambira mumtsinje okha okha kapenanso kuphika pamoto kuopa kuti angadzipweteke okha.
  • Anthu amene amadwala matenda a khunyu asamayendetse galimoto kapena kuyendetsa makina kuopesa kuti angadzivulaze okha kapenso kuvulaza anthu ena.

Tenganipo gawo polpewa zinthu zomwe zimayambitsa kugwa chifufu. Zinthu ngati:

  • Nkhawa komanso mantha
  • Kusagona
  • Kumwa mowa mwauchidakwa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo
  • Magetsi othwanima thwanima
  • Kusakhala ndi nthawi yokhazikika yodyera chakudya zomwe zimapangitsa kuti shuga achepe mthupi

Mankhwala

Palibe mankhwala ochiza Matenda a khunyu. Komano ndi mlingo komanso mankhwala woyenera anthu ambiri amene amadwala matenda a khunyu sagwa chifufu. Mankhwalawa amateteza kuti munthu asamagwe chifufu.

Muyenera kumwa mankwala tsiku ndi tsiku kuti mupewe kugwa chifufu.

Musasiye kapena kuchepesa mankhwala mwazizizi kuopetsa kugwa mowirikiza kapena kumwalira kumene.

Adokotala angathe kuyesa kukusiyitsa mankwala ngati mwakhala wosagwa chifufu pakati pa dzaka ziwiri ndi zitatu.

Ngati chisankho chosiya mankhwala chapangidwa, mulingo wa mankwala uyenera kumachepetsedwa pang’onopang’ono kwa miyezi ingapo. Musasiye kumwa mankhwala panokha popanda kuudzidwa ndi a dokotala.