Psychosis

exp date isn't null, but text field is

Information on Psychosis

What is psychosis?

Psychosis (also called a 'psychotic experience' or 'psychotic episode') is when you perceive or interpret reality in a very different way from people around you. You might be said to 'lose touch' with reality.

Psychosis affects people in different ways. You might experience it once, have short episodes throughout your life, or live with it most of the time (e.g. schizophrenia).

Psychotic disorders are conditions with at least two of the following symptoms:

  • hallucinations (usually hearing voices)
  • delusions (strongly-held, false beliefs, not shared by others in the person’s culture)
  • disorganised behaviour and/or speech (agitation, hyperactivity / inactivity, incoherent / irrelevant speech, signs of self-neglect)

What does psychosis feel like?

Some people have positive experiences of psychosis. For example, if you see the faces of loved ones or hear their voices you may find this comforting. Some people say it helps them understand the world or makes them more creative.

However, for other people psychosis can be a very difficult or frightening experience. You may find that it:

  • affects your behaviour or disrupts your life
  • makes you feel very tired or overwhelmed
  • makes you feel anxious, scared, threatened or confused
  • leaves you finding it very difficult to trust some organisations or people.

It can also be upsetting if people around you dismiss your experiences as untrue when they seem very real to you. You may feel misunderstood and frustrated if other people don't understand. It might help to share our section for friends and family with them.

There are a lot of misunderstandings about what it means to experience psychosis. Lots of people wrongly think that the word 'psychotic' means 'dangerous'. The media often shows people with psychosis behaving like this even though very few people who experience psychosis ever hurt anyone else.

What causes psychosis?

The cause of long-lasting psychotic disorders like schizophrenia is not fully understood but includes genetic factors, early childhood adversity and stressful environmental factors.

Delirium, dementia, severe depression, and drug-induced psychosis are all common causes of psychosis and the treatment is different for all of these conditions.

How can I get help for psychosis?

Many people with schizophrenia now never have to go into hospital and are able to settle down, work and have lasting relationships.

How to Help Myself

It’s important to keep taking your medication unless your doctor advises otherwise. This is true even if you feel well, as the medicine dampens down the symptoms. Stopping the medicine can lead to symptoms returning. Stopping suddenly can have other negative effects too, depending on your specific treatment.

If you have any worries about your medication or its side effects, speak to your doctor. There are usually ways of managing side effects, but if not then other tablets may be available.

Talk to other people with experience of schizophrenia. It can help to know you’re not the only one, and they might be able to offer advice on managing the condition.

Try to stay as physically healthy as possible - eating healthily, exercising and getting enough sleep are also good for keeping mentally well. Some medications can cause weight gain as a side effect, so keep an eye on your weight after starting a new treatment - the team looking after you should do this too.

Symptoms vary a lot between different people. Learn to recognise what happens when you become unwell and be aware of the warning signs. This should be a part of your care plan and it can be useful to share these details with your family.

Uthenga wokhuzana ndi matenda a misala (psychosis)

Kodi misala (psychosis) ndi chani?

Misala (psychosis) ndi matenda omwe amapangitsa munthu kuganiza kapena kuona zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu ena. Anthu amanena kuti munthu yemwe wadwala matenda a misala (psychosis) sakuganizanso ngati mmene umayenera kuganizira.

Matenda a misala (psychosis) amakhudza anthu m’njira zosiyanasiyana. Munthu angathe kudwala kamodzi, kapena kangapo ndithu mmoyo wake, kapena kukhala ndi matendawa moyo wake wonse (monga matenda a misala (psychosis) wotchedwa kuti schizophrenia) kumene.

Matenda a misala (psychosis) amakhala ndi zizindikiro zosachepela ziwiri mwa izi:

  • Kumva, kuona, kununkhiza zinthu zoti palibe (nthawi zambiri kumakhala kumva mau)
  • Zikhulupililo zabodza anngkhale mchikhalidwe chamunthuyo
  • Mkhalidwe osokonekera ndinso kapena mayankhulidwe osokonekera

Kodi matenda a misala (psychosis) amamveka bwanji?

Kwa anthu ena, matenda a misala (psychosis) amawachitira ubwino. Mwachitsanzo ngati munthu akuona nkhope za anthu amene amawakonda kapenanso kumva mawu awo, zimatha kuwakhazika mtima pansi. Anthu ena amati zimawathandiza kumvetsetsa m’mene dziko lilili kapena kuwapangisa kuti akhale ndi danga lomapanga maluso osiyasiyana.

Kwa anthu ena, matenda a misala (psychosis) amabweretsa nyengo yovutitsitsa kapena yoopsa m’moyo mwawo. Matendawa:

  • Amakhudza mkhalidwe komanso kusokoneza moyo wa munthu odwalayo kumene
  • Amapangitsa munthu kutopa kwambiri
  • Amabweretsa mantha, kunjenjemera komanso kusokonekera kumene
  • Amapangisa munthu kusakhulupilira anthu kapena mabungwe.

Zingathenso kukhala zopweteka ngati achibale komanso abwenzi akumatsutsa zomwe zikukuchitikira kumaona ngati nkhamba kamwa pamene kwa iweyo ndizenizeni. Wodwala amatha kuona kuti anthu sakumakumvetsetsa ndipo atha kukhala okhudzidwa ngati anthu ena sakumumvetsa.

Pali kusamvetsetsana kwambiri pakati pa munthu yemwe akudwala matenda a misala (psychosis) ndi anthu ena. Anthu ambiri amakhulupilira kuti misala (psychosis) ndi chinthu choopsa kapena kuti nkhondo. Mauthenga kapena masamba a pa intaneti amakonda kupereka chinthunzithunzi choti matenda a misala (psychosis) ndi nkhondo pamene ndi anthu ochepa chabe omwe amatha kuvulaza anzawo akadwala matenda amisala (psychosis).

Kodi chimayambitsa matenda amisala (psychosis) ndi chani?

Chimene chimayambitsa matenda a misala (psychosis) okhazikika monga a schizophrenia sichimamvetsetseka kwenikweni. Chilengedwe, zokhoma zomwe timakumana nazo kuubwana, komanso zipsinjo mmoyoyu ndi zina mwa zomwe zimatha kuyambitsa matendawa.

Matenda obaizika, matenda am’mutu obwera munthawi yaukalamba, matenda okhumudwa kwambiri, komanso mankhwala ozunguza ubongo ndi zinthu zomwe zimayambitsa misala (psychosis) nthawi zambiri. Thandizo la matenda a misala (psychosis) yoyambitsidwa ndi zinthu izi limakhalanso losiyana.

Kodi thandizo la matenda a misala (psychosis) ndingalipeze bwanji?

Anthu ambiri omwe amadwala matenda a misala (psychosis) ya mgonagona (schizophrenia) samafunikira kugonekedwa kuchipitala ndipo amakhala bwinobwino namagwiranso ntchito zawo ndiponso mmabanja awo.

Ndingadzithandize bwanji ngati ndili ndi matendawa

Nzofunikira kwambiri kupitiliza kumwa mankhwala omwe anakulembelani kuchipatala pokhapokha adokotala anu anena kuti simukuyenera kutero. Izizi n’zoona angakhale mukuziona kapena kudzimva kuti muli bwinobwino. Muli bwino Kamba ka mankhwala omwe azizilitsa matendawa. Kusiya mankhwala kungathe kupangitsa kuti zizindikiro za matendawa zibwerenso. Kungosiya mwazizizi kungabweretsenso mavuto ena malingana ndi mankhwala omwe mukumwa.

Ngati muli ndi madandaulo okhudzana ndi mankhwala anu, kapena mavuto omwe mankhwalawa akubweretsa, afotokozereni adokotala anu. Zilipo njira zothana ndi mavuto obwera Kamba ka mankhwala ndiponso adokotala angathe kusintha mankhwalawo.

Chezani ndi anthu omwe anadwalapo matenda a misala (psychosis). Ndizothandiza kuzindira kuti sindinu nokha amene mwadwalapo matendawa ndipo anthu ena angathe kukupatsani malangizo a momwe mungazithandizire.

Zizindikiro zamatendawa zimasiyana malingana ndi munthu. Yesesani kuzindikira kapena kudziwa zomwe zimachitika ngati kuti mwadwala ndicholinga choti muziwe matendawa akamabwera. Izi ziyenera      kukhala gawo la mmene mumadzitsamalira ndipo adziwitseni achibale.