Self Harm

exp date isn't null, but text field is

Information on Self Harm

What is self-harm?

Self-harm is when someone intentionally damages or injures their body.

There are many different ways people can intentionally harm themselves, such as cutting or burning their skin, punching or hitting themselves and poisoning themselves with tablets or toxic chemicals.

What does self-harm feel like?

Self-harm can help you to feel in control, and reduce uncomfortable feelings of tension and distress. If you feel guilty, it can be a way of punishing yourself and relieving your guilt. Either way, it can become a 'quick fix' for feeling bad.

What causes self-harm?

In most cases, people who self-harm do it to help them cope with overwhelming emotional issues, which may be caused by:

  • Social problems - such as being bullied, having difficulties at work or school, coming to terms with their sexuality, debt or unemployment
  • Trauma - such as physical or sexual abuse, the death of a close family member or friend, or having a miscarriage
  • Psychological problems - such as low self-esteem, having repeated thoughts or voices telling them to self-harm, disassociating (losing touch with who they are and with their surroundings), or borderline personality disorder.

How can I get help for self-harm?

Identify triggers - Self-harm is often a way of dealing with emotional pain, so it is worth trying to identify what feelings make you want to hurt yourself. Once you are aware of your triggers you can take positive steps to reduce or stop the urge to self-harm.

Distract yourself - Distract from the urge to self-harm. Once you know your triggers, you can try and express your feelings in other ways. For example, hitting a pillow can help cope with anger, or having a cold shower can help you stop feeling numb.

Safety plan - Write a ‘safety plan’ for yourself. This could include details on what you can do for yourself, and who you can speak to if you need support. It can help to have something written down, and it is more likely to work because you choose the kind of support you feel most comfortable with.

Lifestyle - Look after your physical health as well as your mental health. Getting enough sleep, eating healthily and exercising regularly can help you feel more positive.

Talk - Ask for help and support. You don’t have to cope with all of your problems alone. It is important to find support. If you’re under 18 speak to adult you can talk to and trust.

Groups - Talk to other people who have had thoughts of self-harm. Their knowledge and experience can be helpful. Organisations such as MeHUCA  (https://www.medcol.mw/mehuca/) can help you to do this.

Tips for families, partners and carers

People often try to keep self-harm secret because of shame or fear of discovery. It's often close family and friends who first notice when somebody is self-harming, and approaching the subject with care and understanding is very important.

If you think a friend or relative is self-harming, look out for any of the following signs:

  • Unexplained cuts, bruises or burns, usually on their arms, wrists, thighs and chest.
  • Keeping themselves fully covered at all times, even in hot weather.
  • Signs of depression, like low mood, tearfulness or a lack of motivation or interest in anything.
  • Self-loathing and expressing a wish to punish themselves.
  • Not wanting to go on and wishing to end it all.
  • Becoming very withdrawn and not speaking to others.
  • Signs of low self-esteem, like blaming themselves for any problems or thinking they’re not good enough for something.
  • Signs they have been pulling out their hair.

They may also have problems with drugs or alcohol, or have issues with eating. People who self-harm can seriously hurt themselves, so it is important to try to encourage them to speak to a healthcare worker about the underlying issue.

Talk to others who care for people who self-harm. They may have experienced similar situations and have useful tips. Organisations such as MeHUCA  (https://www.medcol.mw/mehuca/) can help you to do this.

Uthenga okhudzana ndi kudzivulaza

Kodi kudzivulaza ndichani?

Kudzivulaza ndipamene munthu mwadala akudzivulaza kapena kudzipweteka thupi lake.

Pali njira zambiri zimene anthu angathe kugwiritsa ntchito ndicholinga choti adzivulaze. Zina mwanjirazi ndi monga: kuzicheka kapena kuziotcha khungu, kuzibaya kapena kudzimenya komanso kumwa mankhwala oopsya (poizoni).

Kodi zizindikiro za matendawa ndichani?

Kuzivulaza kungapangitse munthu kuzikhulupilira, komanso kuchepetsa kusamva bwino mmaganizo makamaka munthu ngati ali ndi zipsyinjo. Ngati munthu akudzivera chisoni, kuzivulaza ndi njira imodzi yomwe anthu amagwiritsa ntchito pofuna kudzilanga komanso pofuna kuthetsa kuzimvera chisoniko. Munjira zonsezi, kuzivulaza kungathe kukhala ngati kukonza zinthu msangamsanga chifukwa chodzimvera chisoni.

Kodi chimapangitsa kudzivulaza mwadala ndichani?

Nthawi zambiri anthu amene amazivulaza mwadala amatero ndicholinga choti adzithandize kumva bwino akamadutsa munyengo zowawitsa m’maganizo monga:

  • Mavuto okumana nawo munthu akamakhala ndi anthu ena- monga kunyozedwa, mavuto a kuntchito kapena kusukulu, ngongole, kukhala pa ulova komanso kusintha kwathupi mnyamata kapena mtsikana akamakula.
  • Kuzunguzika kapena kuvulazidwa- mwachitsanzo kuvulazidwa thupi kapenanso kugwiliridwa. Imfa ya abwenzi kapena wachibale angakhalenso mwana akapitilira (kutaya pakati).
  • Mavuto a m’maganizo-monga kusadzikhulupilira, kumva mau a munthu oti palibe kapena kukhala ndi maganizo ozivulaza mwakawirikawiri, kudzipatula (ndi anthu ena omwe munthu amakhala nawo), komanso mkhalidwe wa munthu.

Kodi thandizo la vutoli ndingalipedze bwanji?

Kupedza zomwe zimayambitsa - Kudzivulaza mwadala nthawi zambiri ndi njira yodzithandizira munthu akamamva ululu wa m’maganizo.  Pachifukwachi, nkofunikira kwambiri kupeza zinthu zomwe zimapangitsa kuti munthu akhale ndi maganizo odzivula mwadala.

Munthu akangozindikira zomwe zimabweretsa magizowa, angathe kupanga ndondomeko zabwino zochepetsa kapena zothetsa kumene chilakolako chofuna kuzivulaza mwadala.

Zisokoneze wekha - Zitsokoneze wekha ku chilakolako chofuna kuzivula mwadala. Munthu atha kuyesera kupanga zinthu zina m’malo mozivulaza. Mwachitsanzo, kumenya pilo kungathe kuchepetsa ukali, kapena kusamba madzi ozizila kungathenso kukupangitsa kuti munthu akhale bwino.

Ndondomeko yabwino yozitetezela - Zilembereni nokha ndondomeko yabwino. Zina mwa zomwe zingalembedwe mu ndondomekoyi ndi zinthu zoti ungazipangile wekha, ndiponso munthu amene ungathe kumuuza ngati ukukumana ndi mavuto. Ndondomeko zolembedwa bwino zimathandiza komanso ndidzachidziwikire kuti zimakhala bwino chifukwa munthu amakhala atasankha yekha mtundu wa thandizo lomwe akufuna.

Makhalidwe - Ziyang’anileni moyo wanu wa thupi komanso wa m’magamizo. Kugona mokwanira, kudya chakudya chopatsa thanzi, ndiponso kupanga masewero olimbitsa thupi mwakawirikawiri zimathandiza munthu kukhala ndi moyo wabwino.

Lankhulani - Funani thandizo. Simuyenera kupilira mavuto anu onse panoka. Kupeza thandizo ndichinthu chofunika kwambiri. Ngati simunakwanitse zaka 18, lankhulani ndi munthu wamkulu amene mumamukhulupilira komanso kumumasukira.

Magulu - Afotokozereni anthu ena amene ali ndi mavuto ngati anuwo. Nzeru zawo komanso kuzindikira kwawo kungathe kukhala kothandiza. Magulu ngati la  MeHUCA (https://www.medcol.mw/mehuca/) lingathe kukhala lothandiza.

Zomwe zingathandize kwa mabanja, achibale ndi omwe akuthandiza munthu yemwe ali ndi vutoli.

Nthawi zambiri anthu amasunga mwachinsinsi nkhani zozivulaza mwadala chifukwa cha manyazi komanso mantha. Nthawi zambiri amakhala munthu wachibale kapena abwenzi amene amazindikira kuti munthu wazivulaza mwadala.  Pachifukwachi, kumufikira munthu wozivulazayo mwachikondi ndiponso mwachisamaliro nkofunika kwambiri. Ngati mukuganiza kuti mzanu kapena m’mbale wanu akuzivulaza mwadala, yang’anani zizindikiro izi:

  • Kudzicheka kodabwitsa, kudzikhula pa khungu kapena kupsya kumene. makamaka m’mikono, manja, ntchafu ndi mchifuwa.
  • Ngati munthuyo akuvala moziphimba nthawi zonse angakhale nthawi yotentha.
  • Ngati munthuyo akuonetsa zizindikiro zokhumudwa monga kusasangalala, kulira pafupipafupi, ndiponso kusakhala ndi chilakolako kapena zikhumbokhumbo.
  • Maganizo ofuna kudzilanga.
  • Maganizo ofuna kudzipha.
  • Kudzipatula komanso osalankhula ndi anthu.
  • Zizindikiro zodzikayikila, kudzinamizira mafuvuto, komanso kuziona ngati osachita bwino pa chilichonse.
  • Zizindikro zoti munthuyo akumakoka tsitsi lake.

Angathenso kumagwilitsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo, kumwa mowa mwauchidakwa, komanso amavuta pa nkhani yodya chakudya. Anthu amene amazivulaza mwadala atha kuzipweteka modesa nkhawa kotero nkofunikira kwambiri kuwalimbikitsa kulankhukla ndi adokotala awo pa mavuto omwe akukumana nawo.

Lankhulani ndi anthu ena omwe amathandiza anthu amene amazivulaza mwadala. Angathe kukhala wozindikira pa nkhanizi ndikukhalanso ndi malangizo apadera. Mabungwe ngati MeHUCA (https://www.medcol.mw/mehuca/)  angathe kuthandiza